Judges 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma atsogoleri a ku Sukoti adayankha kuti, “Kodi Zeba ndi Zalimuna waŵagonjetsa kale, m'mene ukuti tiŵapatse buledi ankhondo akoŵa?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna ali m'dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma atsogoleri a Sukoti anayankha kuti, “Kodi Zeba ndi Zalimuna mwawagonjetsa kale kuti tipatse buledi ankhondo akowa?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna ali m'dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate?