Judges 9:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yotamu popitiriza adati, “Kodi tsono mudachita ndi mtima wonse ndiponso mokhulupirika pakumdzoza Abimeleki kuti akhale mfumu? Kodi mwamchitira ulemu Yerubaala ndi banja lake, poyang'anira ntchito zimene adachita?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, ngati mwachita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamchitira chokoma Yerubaala ndi nyumba yake, ndi kumchitira monga anayenera manja ake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yotamu anatinso, “Kodi mukuti munaonetsadi kuona mtima ndi kukhulupirika podzoza Abimeleki kukhala mfumu? Kodi mukuti munachitira ulemu Yeru-Baala ndi banja lake poganizira ntchito zimene anachita?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, ngati mwacita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamcitira cokoma Yerubaala ndi nyumba yace, ndi kumcitira monga anayenera manja ace;