Judges 9:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma lero inu mwaukira banja la bambo wanga. Mwapha ana ake 70 pa mwala umodzi, ndipo mwalonga ufumu Abimeleki, mwana wa mzikazi wake, kuti azilamulira nzika za ku Sekemu, chifukwa chakuti ngwapachibale wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ake, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wake, akhale mfumu ya pa eni ake a ku Sekemu, chifukwa ali mbale wanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma lero inu mwawukira banja la abambo anga. Mwapha ana ake 70 pa mwala umodzi, ndiponso mwalonga ufumu Abimeleki, mwana wa mdzakazi wake kuti akhale wolamulira anthu a ku Sekemu chifukwa ndi mʼbale wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ace, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wace, akhale mfumu ya pa eni ace a ku Sekemu, cifukwa ali mbale wanu;