Judges 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno kuti, ‘Chabwino koposa nchiti kwa inu, kuti ana onse 70 a Yerubaala azikulamulirani, kapena kuti mmodzi yekha azikulamulirani? Muzikumbukiratu kuti paja ine ndine mbale wanu weniweni.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nenanitu m'makutu mwa eni ake onse a ku Sekemu, Chokomera inu nchiti, akulamulireni ana amuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? Mukumbukirenso kuti ine ndine wa fuko lanu ndi nyama yanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno, ‘Chabwino ndi chiyani kwa inu kuti ana onse makumi asanu ndi awiri a Yeru-Baala azikulamulirani, kapena kuti azikulamulirani ndi munthu mmodzi basi?’ Kumbukirani kuti ine ndine mʼbale wanu weniweni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nenanitu m'makutu mwa eni ace onse a ku Sekemu, Cokomera inu nciti, akulamulireni ana amuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? mukumbukilenso kuti ine ndine wa pfuko lanu ndi nyama yanu.