Judges 9:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Izi zidachitika kuti zoipa zimene iye adaŵachita ana 70 a Yerubaala aja zimubwerere, ndipo kuti magazi ao akhale pa Abimeleki mbale wao amene adaŵaphayo, ndiponso pa anthu a ku Sekemu amene adamulimbitsa mtima kuti aphe abale ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti chiwawa adachitira ana amuna makumi asanu ndi awiri a Yerubaala chimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ake a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ake, awaphe abale ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anachita zimenezi kuti zoyipa zimene anachitira ana aamuna 70 a Yeru-Baala aja zimubwerere, ndi kuti magazi awo akhale pa Abimeleki mʼbale wawo ndi pa anthu a ku Sekemu amene anamulimbikitsa mtima kuti aphe abale akewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti ciwawa adacitira ana amuna makumi asanu ndi awiria Yerubaala cimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ace a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ace, awaphe abale ace.