Judges 9:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero anthu a ku Sekemu adaika anthu pamwamba pa mapiri kuti abisalire Abimeleki, ndipo ankaŵalanda zinthu zao anthu onse odzera njira imeneyo. Abimeleki zimenezi adazimva.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo eni ake a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthu a ku Sekemu anayika anthu omubisalira pamwamba pa mapiri. Tsono iwo ankalanda anthu odutsa mʼnjira imeneyo zinthu zawo ndipo Abimeleki anamva zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo eni ace a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.