Judges 9:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adapita ku munda kukathyola mphesa, nafinya mphesazo. Kenaka adachita chikondwerero nakaloŵa m'nyumba ya milungu yao. M'menemo adadya ndi kumwa ndipo adayamba kutukwana Abimeleki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuluka kunka kuminda, natchera mphesa m'mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m'nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo anapita ku munda kukathyola mphesa ndi kuzifinya, ndipo anachita chikondwerero mʼnyumba ya milungu yawo. Anthuwo akudya ndi kumwa, ankatemberera Abimeleki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturuka kumka kuminda, nachera mphesa m'mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m'nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki.