Judges 9:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Gaala, mwana wa Ebedi, adati, “Kodi ife ndife anthu otani m'Sekemu muno? Chifukwa chiyani tikutumikira Abimeleki? Ndipo kodi ndaninso amene uja? Ha, si mwana wa Gideoni! Zebuli amalamulidwa ndi iye uja, koma nanga ife kuti tizimtumikira nchifukwa chiyani? Tiyeni tikhale pambuyo pa kholo lathu Hamori, tate wa fuko lathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? Sindiye mwana wa Yerubaala kodi? Ndi Zebuli kazembe wake? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire chifukwa ninji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Gaali mwana wa Ebedi anati “Kodi Abimeleki ndi ndani, ndipo nʼchifukwa chiyani akutilamulira ife Asekemu? Kodi iyeyu si mwana wa Yeru-Baala ndipo womuthandiza wake si Zebuli? Tiyeni titumikire anthu a ku Hamori, kholo la fuko la Sekemu! Nanga nʼchifukwa chiyani tikutumikira Abimeleki?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? sindiye mwana wa Yerubaala kodi? ndi Zebuli kazembe wace? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire cifukwa ninji?