Judges 9:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono m'maŵa dzuŵa likamatuluka, mudzuke msanga, mukauthire nkhondo mzindawo. Pamene Gaalayo ndi anthu ake azibwera kudzalimbana nanu, muŵakanthe monga m'mene mungathere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo kukhale kuti m'mawa, pakutuluka dzuwa, muuke mamawa mugwere mudziwo; ndipo taonani, akakutulukirani iye ndi anthu ali naye, uzimchitira monga lidziwa dzanja lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa dzuwa likutuluka, mudzuke ndi kukathira nkhondo mzindawo. Gaali ndi anthu amene ali naye akamadzabwera kuti alimbane ndi inu, inu mudzathane nawo monga mmene mungachitire.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo kukhale kuti m'mawa, pakuturuka dzuwa, muuke mamawa mugwere mudziwo; ndipo taonani, akakuturukirani iye ndi anthu ali naye, uzimcitira monga lidziwa dzanja lako.