Judges 9:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gaala mwana wa Ebedi adatuluka nakaima pa khomo la chipata cha mzinda. Ndipo Abimeleki ndi anthu ake adavumbuluka kumene adabisala kuja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anatuluka, naima polowera pa chipata cha mudzi; naika Abimeleki ndi anthu anali naye m'molalira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gaali mwana wa Ebedi anatuluka nakayima pa khomo pa chipata cha mzinda pamene Abimeleki ndi ankhondo ake anatuluka ku malo kumene anabisala kuja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anaturuka, naima polowera pa cipata ca mudzi; nauka Abimeleki ndi anthu anali naye m'molalira.