Judges 9:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Gaala ataŵaona anthuwo, adauza Zebuli kuti, “Ona, anthu akutsika kuchokera pamwamba pa mapiri.” Zebuli adayankha kuti, “Si anthu amenewo, ndi zithunzithunzi chabe zapamapiri zonga anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Gaala anapenya anthuwo anati kwa Zebuli, Taona, alikutsika anthu kuchokera pamwamba pa mapiri. Koma Zebuli ananena naye, Uona mthunzi wa mapiri ndi kuyesa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gaaliyo atawaona, anawuza Zebuli kuti, “Taona anthu akutsika kuchoka pamwamba pa mapiri.” Koma Zebuli anayankha kuti, “Zimene mukuonazo ndi zithunzi za mapiri chabe osati anthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Gaala anapenya anthuwo anati kwa Zebuli, Taona, alikutsika anthu kucokera pamwamba pa mapiri, Koma Zebuli ananena naye, Uona mthunzi wa mapiri ndi kuyesa anthu.