Judges 9:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adampatsa ndalama zasiliva 70 za m'nyumba yachipembedzo ya Baala wa Chipangano. Ndalama zimenezo Abimeleki uja adaalembera anthu aganyu achabechabe ndi osasamala ntchito kuti azimtsata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-Beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pake ndi opepuka amene anamtsata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anamupatsa ndalama zasiliva 70 za mʼnyumba ya chipembedzo ya Baala Beriti. Ndi ndalama zimenezi Abimeleki analemba anthu achabechabe ndi osasamala kuti azimutsatira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pace ndi opepuka amene anamtsata.