Judges 9:48 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adapita ku phiri la Zalimuna ndi anthu ake onse. Kumeneko adatenga nkhwangwa m'manja mwake nadula nthambi za mtengo, ndipo adazinyamula nazisenza pa phewa. Tsono adauza anthu akewo kuti, “Zimene mwaona ndikuchitazi, fulumirani inunso muchite chimodzimodzi, monga momwe ndachitira inemu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Abimeleki anakwera kunka kuphiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m'dzanja lake Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kuiika paphewa pake, nati kwa anthu okhala naye, Ichi munachiona ndachita, fulumirani, muchite momwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Abimeleki pamodzi ndi anthu ake onse anapita ku phiri la Zalimoni. Kumeneko anatenga nkhwangwa nadula nthambi za mitengo. Ananyamula nthambi zija pa phewa pake. Tsono anawuza anthu aja kuti, “Zimene mwaona ine ndikuchita, inunso mufulumire kuchita monga ndachitiramu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Abimeleki anakwera kumka ku phiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m'dzanja lace Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kulika paphewa pace, nati kwa anthu okhala naye, Ici munaciona ndacita, fulumirani, mucite momwemo.