Judges 9:49 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho aliyense adadula mtolo wake natsatira Abimeleki, nakayedzeka mtolo wakewo pa linga lija ndipo adaliyatsa moto, kotero kuti anthu onse a ku nsanja ya Sekemu adafa. Analipo anthu ngati chikwi chimodzi, amuna ndi akazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi anthu onse anadulanso yense nthambi yake, natsata Abimeleki, naziika pangaka, natentha nazo ngakayo ndi moto; motero anthu onse a nsanja ya ku Sekemu anafanso, amuna ndi akazi ngati chikwi chimodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono aliyense anadula nthambi zake, natsatira Abimeleki. Anakawunjika nthambi zija pa linga paja, kenaka ndi kuliyatsa moto. Choncho anthu onse a ku nsanja ya Sekemu anafa. Analipo anthu pafupifupi 1,000, amuna ndi akazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi anthu onse anadulanso yense nthambi yace, natsata Abimeleki, naziika pangaka, natentha nazo ngakayo ndi moto; motero anthu onse a nsanja ya ku Sekemu anafanso, amuna ndi akazi ngati cikwi cimodzi.