Judges 9:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapita ku nyumba ya bambo wake ku Ufura, nakaŵaphera pa mwala umodzi abale ake 70, ana a Yerubaala. Koma Yotamu, mzime wa Yerubaala, sadaphedwe nao chifukwa adaabisala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapita ku Ofiri ku mudzi kwa abambo ake ndipo anapha abale ake makumi asanu ndi awiri, ana a Yeru-Baala pa mwala umodzi. Koma Yotamu yemwe anali wamngʼono mwa onsewo anapulumuka chifukwa anabisala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuka ku nyumba ya atate wace ku Ofira, nawapha abale ace ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.