Judges 9:54 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Abimeleki uja adaitana msangamsanga mnyamata wake womunyamulira zida zake zankhondo namuuza kuti, “Solola lupanga lako, unditsirize, sindifuna kuti anthu azikati, ‘Mkazi ndiye amene adamupha.’ ” Apo mnyamata wakeyo adambayadi ndi lupanga, mpaka kutulukira kunja lupangalo, naafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwamsanga Abimeleki anayitana mnyamata womunyamulira zida za nkhondo namuwuza kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuti anthu asadzanene kuti, ‘Mkazi ndiye anamupha.’ ” Choncho wantchito wake anamubayadi mpaka kutulukira kunja lupangalo ndipo anafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaitana msanga mnyamata wace wosenza zida zace, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wace, nafa iye.