Judges 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono nzika zonse za ku Sekemu zidasonkhana ndi anthu a ku nyumba ya Betemilo, nkupita ku mtengo wa thundu pafupi ndi chipilala chachipembedzo cha ku Sekemu, kukalonga Abimeleki ufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anasonkhana eni ake onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa choimiritsa chili m'Sekemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono nzika za ku Sekemu ndi za ku Beti-Milo zinapita kukasonkhana ku mtengo wa thundu pafupi ndi chipilala cha ku Sekemu kuti akalonge Abimeleki ufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anasonkhana eni ace onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa coimiritsa ciri m'Sekemu.