Lamentations 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ake onse amabuula akamafunafuna chakudya. Chuma chao amagulitsana ndi chakudya, kuti apezenso mphamvu. Akuti, “Inu Chauta penyani, muwone m'mene akundinyozera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate; ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ake onse akubuwula pamene akufunafuna chakudya; asinthanitsa chuma chawo ndi chakudya kuti akhale ndi moyo. “Inu Yehova, taonani ndipo ganizirani, chifukwa ine ndanyozeka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu ace onse ausa moyo nafunafuna mkate; Ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; Taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.