Lamentations 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu amene mukudutsanu? Tangopenyani, muwone ngati pali mavuto ena onga angaŵa, mavuto amene Chauta adandigwetsamo, pamene adandikwiyira koopsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi muyesa chimenechi chabe, nonsenu opita panjira? Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni china ngati changachi amandimvetsa ine, chimene Yehova wandisautsa nacho tsiku la mkwiyo wake waukali?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu nonse mukudutsa? Yangʼanani ndipo muone. Kodi pali mavuto ofanana ndi amene andigwerawa, amene Ambuye anandibweretsera pa tsiku la ukali wake?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi muyesa cimeneci cabe, nonsenu opita panjira? Penyani nimuone, kodi ciripo cisoni cina ngati cangaci amandimvetsa ine, Cimene Yehova wandisautsa naco tsiku la mkwiyo wace waukali?