Lamentations 1:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatumiza moto kuchokera Kumwamba. Udaloŵa mpaka m'kati mwa mafupa anga. Adayala ukonde kuti akole mapazi anga, nandibweza. Adandisiya ndili ndi chisoni chachikulu, ndili wolefuka tsiku lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anatumiza moto wochokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa; watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo; wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anatumiza moto kuchokera kumwamba, unalowa mpaka mʼmafupa anga. Anayala ukonde kuti ukole mapazi anga ndipo anandibweza. Anandisiya wopanda chilichonse, wolefuka tsiku lonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anatumiza moto wocokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa; Wachera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo; Wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.