Lamentations 1:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zolakwa zanga adazimanga pamodzi kuti zikhale ngati goli. Adazimanga ndi manja ake. Adazimangirira m'khosi mwanga, adafooketsa mphamvu zanga. Chauta wandipereka kwa anthu amene sindingathe kulimbana nawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake; zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvu yanga; Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwalaka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Wazindikira machimo anga onse ndipo ndi manja ake anawaluka pamodzi. Machimowa afika pakhosi panga, ndipo Ambuye wandithetsa mphamvu. Iye wandipereka kwa anthu amene sindingalimbane nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Gori la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lace; Zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvuyanga; Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwalaka.