Lamentations 1:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaŵamwaza anthu anga onse amphamvu amene ankakhala nane. Adasonkhanitsa gulu lina la anthu kuti liwononge anyamata anga. Chauta adapondereza Ayuda, anthu ake opatulika, monga m'mene anthu amachitira mphesa mopondera mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye wapepula ngwazi zanga zonse pakati panga; waitanira msonkhano pa ine kuti uphwanye anyamata anga, Ambuye wapondereza namwaliyo, mwana wamkazi wa Yuda, monga mopondera mphesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ambuye wakana anthu anga onse amphamvu omwe ankakhala nane: wasonkhanitsa gulu lankhondo kuti lilimbane nane, kuti litekedze anyamata anga; mʼmalo ofinyira mphesa Ambuye wapondereza anamwali a Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye wapepula ngwazi zanga zonse pakati panga; Waitanira msonkhano pa ine kuti uphwanye anyamata anga, Ambuye wapondereza namwaliyo, mwana wamkazi wa Ziyoni, monga mopondera mphesa.