Lamentations 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa cha zimenezi ndikulira, misozi ili mbwembwembwe m'masomu. Pakuti wondisangalatsa sali pafupi, wondilimbitsa mtima ali kutali. Anthu anga asiyidwa chifukwa mdani watigonjetsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Chifukwa cha zimenezi ndikulira ndipo maso anga adzaza ndi misozi. Palibe aliyense pafupi woti anditonthoze, palibe aliyense wondilimbitsa mtima. Ana anga ali okhaokha chifukwa mdani watigonjetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditarikira; Ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.