Lamentations 1:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukungolira usiku wonse, misozi ikungoti mbwembwembwe pamasaya pake. Mwa onse amene ankaukonda, palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala woti aziwusangalatsa. Abwenzi ake onse auchita zaupandu, onse asanduka adani ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ukulira mowawidwa mtima usiku wonse, misozi ili pa masaya pake. Mwa abwenzi ake onse, palibe ndi mmodzi yemwe womutonthoza. Abwenzi ake onse amuchitira chiwembu; onse akhala adani ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uliralira usiku; misozi yace iri pa masaya ace; Mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ace onse aucitira ziwembu, Asanduka adani ace.