Lamentations 1:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani Inu Chauta m'mene ndavutikira mumtima mwanga, moyo wanga wazunzika zedi. Mtima wanga wakongonyala, chifukwa choti ndapanduka kwambiri. Mu mseu anthu akuphedwa ndi lupanga, m'nyumbanso ndi imfa yokhayokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onani, Yehova; pakuti ndavutika, m'kati mwanga mugwedezeka; mtima wanga wasanduka mwa ine; pakuti ndapikisana nanu ndithu; kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu Yehova, onani mmene ine ndavutikira! Ndikuzunzika mʼkati mwanga, ndipo mu mtima mwanga ndasautsidwa chifukwa ndakhala osamvera. Mʼmisewu anthu akuphedwa, ndipo ku mudzi kuli imfa yokhayokha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onani, Yehova; pakuti ndabvutika, m'kati mwanga mugwedezeka; Mtima wanga wasanduka mwa ine; pakuti ndapikisana nanu ndithu; Kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.