Lamentations 1:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu akundimva pamene ndikudandaula, koma palibe wondisangalatsa. Adani anga onse atamva za tsoka langa, adakondwa chifukwa cha zimene mudachita. Tsiku limene mudalonjeza lija mulifikitse ndithu. Nawonso adzasauke ngati ine ndemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo anamva kuti ndiusa moyo, palibe wonditonthoza; adani anga onse atha kumva msauko wanga, nakondwera kuti mwatero ndinu; mudzafikitsa tsiku lija mwalitchula, ndipo iwowo adzanga ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu amva kubuwula kwanga, koma palibe wonditonthoza. Adani anga onse amva masautso anga; iwo akusangalala pa zimene Inu mwachita. Lifikitseni tsiku limene munalonjeza lija kuti iwonso adzakhale ngati ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo anamva kuti ndiusa moyo, palibe wonditonthoza; Adani anga onse atha kumva msauko wanga, nakondwera kuti mwatero ndinu; Mudzafikitsa tsiku lija mwalichula, ndipo iwowo adzanga ine.