Lamentations 1:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ntchito zao zonse zoipa mudzaŵaimbe nazo mlandu. Muŵalange monga mudandilangira ine chifukwa cha zolakwa zanga zonse. Ndikubuula kwambiri, ndipo mtima wanga wafookeratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zoipa zao zonse zidze pamaso panu, muwachitire monga mwandichitira ine chifukwa cha zolakwa zanga zonse, pakuti ndiusa moyo kwambiri, ndi kulefuka mtima wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Lolani kuti ntchito zawo zoyipa zifike pamaso panu; muwalange ngati mmene mwandilangira ine chifukwa cha machimo anga onse. Ndikubuwula kwambiri ndipo mtima wanga walefuka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zoipa zao zonse zidze pamaso panu, Muwacitire monga mwandicitira ine cifukwa ca zolakwa zanga zonse, Pakuti ndiusa moyo kwambiri, ndi kulefuka mtima wanga,