Lamentations 1:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ayuda apita ku ukapolo kukazunzika, ndi kukagwira ntchito yakalavulagaga. Akukhala m'maiko ena, osaona malo opumulira. Onse oŵapirikitsa aŵapeza, ali pa mavuto zedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yuda watengedwa ndende chifukwa cha msauko ndi ukapolo waukulu; akhala mwa amitundu, sapeza popuma; onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yuda watengedwa ku ukapolo, kukazunzika ndi kukagwira ntchito yolemetsa. Iye akukhala pakati pa anthu a mitundu ina; ndipo alibe malo opumulira. Onse omuthamangitsa iye amupitirira, ndipo alibe kwina kothawira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yuda watengedwa ndende cifukwa ca msauko ndi ukapolo waukuru; Akhala mwa amitundu, sapeza popuma; Onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza.