Lamentations 1:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Miseu yopita ku Ziyoni yaŵirira, chifukwa palibe wopitako kuti akapembedze pa masiku achikondwerero. Zipata zake zonse zili pululu, ansembe ake akungodandaula. Anamwali ake aja mtima wao ukupweteka, ndithu Ziyoni ali pa masautso oopsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano; pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo; anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Misewu yopita ku Ziyoni ikulira, chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe akubwera ku maphwando ake. Zipata zake zonse zili pululu, ansembe akubuwula. Anamwali ake akulira, ndipo ali mʼmasautso woopsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano; Pa zipata zace zonse papasuka; ansembe ace onse ausa moyo; Anamwali ace asautsidwa; iye mwini namva zowawa.