Lamentations 1:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adani ake asanduka omulamulira, odana naye akupeza bwino, popeza kuti Chauta wamugwetsa m'mavuto chifukwa cha machimo ochuluka a anthu ake. Ana ake amuchokera, atengedwa ukapolo ndi adani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amaliwongo ake asanduka akulu ake, adani ake napindula; pakuti Yehova wamsautsa pochuluka zolakwa zake; ana ake ang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adani ake asanduka mabwana ake; odana naye akupeza bwino. Yehova wamubweretsera mavuto chifukwa cha machimo ake ambiri. Ana ake atengedwa ukapolo pamaso pa mdani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amaliwongo ace asanduka akuru ace, adani ace napindula; Pakuti Yehova wamsautsa pocuruka zolakwa zace; Ana ace ang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ace.