Lamentations 1:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ulemerero wonse wa Ziyoni wachokeratu. Akalonga ake asanduka ngati mphoyo zosoŵa msipu. Ankathaŵa opanda ndi mphamvu zomwe, pofika adani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ulemu wake wonse wamchokera mwana wamkazi wa Ziyoni; akalonga ake asanduka nswala zosapeza busa, anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompirikitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ulemerero wonse wa mwana wamkazi wa Ziyoni wachokeratu. Akalonga ake ali ngati mbawala zosowa msipu; alibe mphamvu zothawira owathamangitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ulemu wace wonse wamcokera mwana wamkazi wa Ziyoni; Akalonga ace asanduka nswala zosapeza busa, Anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompitikitsa.