Lamentations 1:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku a mavuto ake ndi a kuzunzika kwake, Yerusalemu amakumbukira zabwino zonse zimene anali nazo masiku amakedzana. Pamene anthu ake adagwa m'manja mwa adani, panalibe womuthandiza. Adani ake ankamupenyetsetsa monyodola namaseka kugwa kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'masiku a msauko wake ndi kusochera kwake Yerusalemu ukumbukira zokondweretsa zake zonse zachikhalire; pogwidwa anthu ake ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa, mdaniwo anamuona naseka mwachipongwe mabwinja ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa masiku a masautso ndi kuzunzika kwake, Yerusalemu amakumbukira chuma chonse chimene mʼmasiku amakedzana chinali chake. Anthu ake atagwidwa ndi adani ake, panalibe aliyense womuthandiza. Adani ake ankamuyangʼana ndi kumuseka chifukwa cha kuwonongeka kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'masiku a msauko wace ndi kusocera kwace Yerusalemu ukumbukira zokondweretsa zace zonse zacikhalire; Pogwidwa anthu ace ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa, Adaniwo anamuona naseka mwacipongwe mabwinja ace.