Lamentations 1:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yerusalemu adachimwa kwambiri, motero wasanduka wonyansa. Onse amene ankamulemekeza, akumunyoza tsopano, chifukwa aona maliseche ake. Iyeyo akungobuula ndipo akuyang'ana kumbali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yerusalemu wachimwa kwambiri; chifukwa chake wasanduka chinthu chonyansa; onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamaliseche; inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yerusalemu wachimwa kwambiri ndipo potero wakhala wodetsedwa. Onse amene ankamulemekeza pano akumunyoza, chifukwa aona umaliseche wake. Iye mwini akubuwula ndipo akubisa nkhope yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yerusalemu wacimwa kwambiri; cifukwa cace wasanduka cinthu conyansa; Onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamarisece; Inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.