Lamentations 1:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uve wake unkaonekera poyera, iye osaganizako za tsoka lake lakutsogolo. Nchifukwa chake kugwa kwake kunali koopsa, ndipo panalibe womuthuzitsa mtima. Akungoti, “Inu Chauta, muyang'ane mavuto anga, pakuti adani anga apambana.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udyo wake unali m'nsalu zake; sunakumbukira chitsiriziro chake; chifukwa chake watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza; taonani, Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuza yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uve wake umaonekera pa zovala zake; iye sanaganizire za tsogolo lake. Nʼchifukwa chake kugwa kwake kunali kwakukulu; ndipo analibe womutonthoza. “Inu Yehova, taonani masautso anga, pakuti mdani wapambana.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udio wace unali m'nsaru zace; sunakumbukira citsiriziro cace; Cifukwa cace watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza; Taonani Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuzayekha.