Lamentations 2:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta wakwiya kwambiri, taonani m'mene waphimbira Ziyoni ndi mdima! Ulemerero wa Israele wautaya pansi kuuchotsa Kumwamba. Pa tsiku la mkwiyo wake sadakumbukirenso kuti Ziyoni anali ngati mphondero yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Haa, Ambuye waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni ndi mtambo wa mkwiyo wake! Iye wataya pansi ulemerero wa Israeli kuchoka kumwamba. Pa tsiku la mkwiyo wake Iye sanakumbukirenso popondapo mapazi ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kucokera kumwamba kukoma kwace kwa Israyeli; Osakumbukira poponda mapazi ace tsiku la mkwiyo wace.