Lamentations 2:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuluakulu a mu mzinda wa Ziyoni, akhala pansi atangoti chete. Adzithira fumbi kumutu, ndipo avala ziguduli. Anamwali a ku Yerusalemu aŵeramitsa mitu yao pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola; aponya fumbi pa mitu yao, anamangirira chiguduli m'chuuno mwao: Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala chete pansi; awaza fumbi pa mitu yawo ndipo avala ziguduli. Anamwali a Yerusalemu aweramitsa mitu yawo pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola; Aponya pfumbi pa mitu yao, namangirira ciguduli m'cuuno mwao: Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.