Lamentations 2:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maso anga atopa nkulira, moyo wanga wazunzika zedi, Mumtima mwanga mwadzaza chisoni, chifukwa choti anthu anga aonongeka, ana ndi makanda omwe akukomoka m'miseu yamumzinda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasula kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maso anga atopa ndi kulira, ndazunzika mʼmoyo mwanga, mtima wanga wadzaza ndi chisoni chifukwa anthu anga akuwonongeka, chifukwa ana ndi makanda akukomoka mʼmisewu ya mu mzinda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; Ciwindi canga cagwa pansi cifukwa ca kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu amtundu wanga; Cifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.