Lamentations 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anawo akufunsa amai ao kuti, “Kodi chakudya ndi chakumwa tingazipeze kuti?” Akufunsa zimenezi pamene akukomoka m'miseu yamumzinda ngati anthu olasidwa. Akuthatha ndi moyo pa mfukato wa amai ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti? Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu, potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawo akufunsa amayi awo kuti, “Kodi tirigu ndi vinyo zili kuti?” pamene akukomoka ngati anthu olasidwa mʼmisewu ya mʼmizinda, pamene miyoyo yawo ikufowoka mʼmanja mwa amayi awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti? Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu, Potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.