Lamentations 2:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe mzinda wa Yerusalemu, ndinganene chiyani za iwe, kaya nkukuyerekeza ndi chiyani? Iwe mzinda wangwiro wa Ziyoni, kodi ndingakufanizire ndi yani, kuti choncho ndikusangalatse? Kuwonongeka kwako nkwakukulu ngati nyanja. Ndani angathe kukukonzanso?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinganene chiyani za iwe? Ndingakufanizire ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu? Kodi ndingakufanizire ndi yani kuti ndikutonthoze, iwe namwali wa Ziyoni? Chilonda chako ndi chozama ngati nyanja, kodi ndani angakuchiritse?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikucitire umboni wotani? ndikuyerekeze ndi ciani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi ciani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakucize?