Lamentations 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zinthu zimene aneneri ako adakuwonera m'masomphenya zinali zabodza ndi zonyenga. Iwo sadaonetse uchimo wako, kuti ukhalenso pabwino. Mau amene adakutengeraniwo anali abodza ndi osokeretsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aneneri ako anakuonera masomphenya achabe ndi opusa; osawulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako, koma anakuonera manenero achabe ndi opambutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masomphenya a aneneri ako anali abodza ndi achabechabe. Iwo sanakupulumutse kuti usapite ku ukapolo poyika poyera mphulupulu zako. Mauthenga amene anakupatsa anali achabechabe ndi osocheretsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aneneri ako anakuonera masomphenya acabe ndi opusa; Osaulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako, Koma anakuonera manenero acabe ndi opambutsa.