Lamentations 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse odutsa m'njira akukuwombera m'manja mokunyodola. Akukutsonya ndi kukupukusira mitu, iwe mzinda wa Yerusalemu. Akunena kuti, “Kodi mzinda uja ndi uwu umene kale lija ankautcha wodala kotheratu, mzinda wokondweretsa dziko lonse lapansi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onse opita panjira akuombera manja: Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati, kodi uwu ndi mudzi wotchedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse oyenda mʼnjira yako akukuwombera mʼmanja; akugwedeza mitu yawo ndi kukunyodola iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu: “Kodi mzinda uja ndi uwu umene unkatchedwa wokongola kotheratu, chimwemwe cha dziko lonse lapansi?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onse opita panjira akuombera manja: Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati, Kodi uwu ndi mudzi wochedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?