Lamentations 2:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adani ako onse akukuyasamira kukamwa mwaukali, ndipo akukunyodola. Akukutsonya ndi kumakukuta mano ao namanena kuti, “Tafikapodi pousakaza! Ah! Tsiku lija tinkafunali ndi lero. Tagonera, taliwonadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adani ako onse akutsekulira pakamwa ndi kukunyoza; iwo akunyogodola ndi kukukuta mano awo, ndipo akuti, “Tamumeza. Tsiku ili ndi lomwe timayembekezera; tili ndi moyo kuti tilione.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adani ako onse ayasamira pa iwe, Atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; Ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.