Lamentations 2:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta wachitadi zimene adakonzekera kuti achite. Wachitadi zimene ankanena moopseza. Monga momwe adaakonzeratu masiku amakedzana, wakuwononga mopanda chifundo, walola adani kuti akondwe chifukwa cha tsoka lako, ndipo wakulitsa kwambiri mphamvu za adani ako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wachita chomwe analingalira; watsiriza mau ake, amene analamulira nthawi yakale; wagwetsa osachitira chisoni; wakondweretsa adani pa iwe, wakweza nyanga ya amaliwongo ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova wachita chimene anakonzeratu; wakwaniritsa mawu ake, amene anatsimikiza kale lomwe. Wakuwononga mopanda chifundo, walola mdani kuti akondwere chifukwa cha kugwa kwako, wakweza mphamvu za adani ako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wacita comwe analingalira; Watsiriza mau ace, amene analamulira nthawi yakale; Wagwetsa osacitira cisoni; Wakondweretsa adani pa iwe, Wakweza nyanga ya amaliwongo ako.