Lamentations 2:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Fuulani kwamphamvu kwa Ambuye, inu anthu a ku Ziyoni. Misozi yanu ichite kuti yoyoyo, ngati mtsinje, usana ndi usiku. Musadzipatse nthaŵi yoti mupumule. Misozi yanu isalekeze.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mtima wao unafuula kwa Ambuye, linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni, igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku; usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitima ya anthu ikufuwulira Ambuye. Iwe khoma la mwana wamkazi wa Ziyoni, misozi yako itsike ngati mtsinje usana ndi usiku; usadzipatse wekha mpumulo, maso ako asaleke kukhetsa misozi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mtima wao unapfuula kwa Ambuye, Linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni, igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku; Usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.