Lamentations 2:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzukani, ndipo mufuule usiku pachiyambi penipeni pa maulonda. Nenani zanu zonse zakukhosi pamaso pa Ambuye. Kwezani manja ndi kupemphera kwa Ambuyewo chifukwa cha moyo wa ana anu amene akukomoka ndi njala m'miseu yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tauka, tafuula usiku, poyamba kulonda; tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye; takwezera maso ako kwa Iye, chifukwa cha moyo wa tiana tako, timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzuka, fuwula usiku, pamene alonda ayamba kulondera; khuthula mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye. Kweza manja ako kwa Iye chifukwa cha miyoyo ya ana ako, amene akukomoka ndi njala mʼmisewu yonse ya mu mzinda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tauka, tapfuula usiku, poyamba kulonda; Tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye; Takwezera maso ako kwa Iye, cifukwa ca moyo wa tiana tako, Timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.