Lamentations 2:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta onani, ndipo mupenye! Kodi ndani amene Inu mwamuvuta chotereyu? Kodi akazi achite kudya ana ao, ana amene iwo omwe adaŵalera bwino? Nanga ansembe ndi aneneri, kodi achite kuŵaphera m'malo opatulika a Ambuye?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawalera wokha? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova, onani, ndipo ganizirani: kodi ndani amene mwamuchitirapo zinthu ngati izi? Kodi amayi adye ana awo, amene amawasamalira? Kodi ansembe ndi aneneri awaphere mʼmalo opatulika a Ambuye?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onani Yehova, nimupenye, mwacitira ayani ici? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawaseweza? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?