Lamentations 2:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anyamata ali gonegone m'miseu pamodzi ndi nkhalamba zomwe. Anamwali anga ndi anyamata anga aphedwa ndi nkhondo. Mwaŵapha pa tsiku la mkwiyo wanu, mwaŵapha mopanda chifundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala; anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga; munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osachitira chisoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anyamata ndi okalamba aligone pamodzi pa fumbi la mʼmisewu ya mu mzinda; anyamata anga ndi anamwali anga aphedwa ndi lupanga. Inu Yehova mwawapha pa tsiku la mkwiyo wanu; mwawapha mopanda chifundo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala; Anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga; Munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osacitira cisoni.