Lamentations 2:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe mumaitanira ku chikondwerero, ndi m'mene mwandiitanira zoopsa kuchokera mbali zonse. Inu Chauta, pa tsiku la mkwiyo wanu, palibe amene adathaŵako kapena kupulumuka. Onse amene ndidaŵabala ndi kuŵalera, adani anga adaŵaononga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwaitana zondiopsa mozungulira ngati tsiku la msonkhano; panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova; omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati momwe mumayitanira pa tsiku la phwando, chimodzimodzinso mwandiyitanira zoopsa mbali zonse. Pa tsiku limene Yehova wakwiya palibe amene angathawe ndi kukhala ndi moyo; mdani wanga wawononga onse amene ndinkawasamala ndi kuwalera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwaitana zondiopsya mozungulira ngati tsiku la msonkhano; Panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova; Omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.