Lamentations 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta atapsa mtima adathyola nyonga zomwe ankanyadira Israele. Adabweza dzanja lake loteteza, adani atayandikira. Mkwiyo wake udalanga fuko la Yakobe ngati moto walaŵilaŵi wonka nuwononga zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pokwiya moopsa walikha nyanga zonse za Israele; wabweza m'mbuyo dzanja lake lamanja pamaso pa adaniwo, natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atakwiya kwambiri, Ambuye anathyola nyanga iliyonse ya Israeli. Anabweza dzanja lake lamanja pamene mdani anamuyandikira. Ambuye anatentha fuko la Yakobo ngati moto wonyeketsa umene umawononga zinthu zonse zomwe zili pafupi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pokwiya moopsya walikha nyanga zonse za Israyeli; Wabweza m'mbuyo dzanja lace lamanja pamaso pa adaniwo, Natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.