Lamentations 2:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalozetsa mivi yake kwa ife ngati mdani wathu, wasamuladi dzanja ngati mdani. Adapha onse amene tinkaŵayang'ana monyadira, pakati pa anthu a mu mzinda wa Ziyoni. Ukali wake unkachita kuyaka ngati moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wathifula uta wake ngati mdani, waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo; wapha onse okondweretsa maso; watsanulira ukali wake ngati moto pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wakokera uta wake pa ife ngati ndife adani; wayimiritsa dzanja lake pa ife ngati ndife adani, ndipo anapha onse amene tinkawayangʼana monyadira. Ukali wake ukuyaka ngati moto pa tenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wathifula uta wace ngati mdani, waima ndi dzanja lace lamanja ngati mmaliwongo; Wapha onse okondweretsa maso; Watsanulira ukali wace ngati moto pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.